R.A YAYIMITSA KUTSEKA KWA MSEWU WA CHIWETA
Bungwe la Roads Authority (RA) lalengeza kuti ntchito yotseka msewu wa M001 ku Chiweta mu Boma la Rumphi yomwe imayenera kuchitika Lachisanu pa 16 October 2026, yayimitsidwa.
Malinga ndi chidziwitso chomwe bungweli linatulutsa lolemba pa 12 October 2026, msewuwu umayenera kutsekedwa kwa kanthawi kochepa "maola awiri" chifukwa cha ntchito yophulitsa miyala mwadongosolo, lero bungwli latilutsa chikalata chodziwitsa kulepheleka kwa chokonzerochi.
RA yati msewuwu udzakhala wotseguka monga mwa nthawi zonse.
RA yati tsiku ntchitoyilatsopano la lidzalengezedwa mtsogolomo.
Bungweli lapepesa kwa onse ogwiritsa ntchito msewuwu pa vuto lililonse lomwe chisankhochi lidadza kamba ka chikonzerochi, ndipo layamika anthu chifukwa cha kumvetsetsa kwawo.
Izi zikutanthauza kuti magalimoto oyenda pakati pa Karonga ndi Rumphi adutsa pa Chiweta popanda choletsa chilichonse Lachisanu.
Comments
Post a Comment